1 Kings 18:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ahabu ataona Eliya, adamuuza kuti, “Ha, iwe munthu wovuta anthu a ku Israele, wabweradi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika pamene Ahabu anaona Eliya, Ahabu anati kwa iye, Kodi ndiwe uja umavuta Israeleyo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Ahabu anaona Eliya, anati kwa iye, “Kodi ndiwedi, munthu wovutitsa Israeli uja?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika pamene Ahabu anaona Eliya, Ahabu anati kwa iye Kodi ndiwe uja umbvuta Israyeliyo?