1 Kings 18:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake tsopano tumizani mau kuti musonkhanitse onse a ku Israele, kuti abwere, ndikakumane nawo ku Phiri la Karimele. Abwere ndi aneneri a Baala 450, ndiponso aneneri a fano la Asera 400, amene amadya kwa Yezebele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisraele onse kuphiri la Karimele, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a chifanizocho mazana anai, akudya pa gome la Yezebele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano sonkhanitsani anthu a mʼdziko lonse la Israeli kuti akumane nane pa Phiri la Karimeli. Ndipo mubwere nawo aneneri a Baala 450 ndi aneneri a fano la Asera 400, amene amadya pa tebulo la Yezebeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisrayeli onse ku phiri la Karimeli, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a cifanizoco mazana anai, akudya pa gome la Yezebeli.