1 Kings 18:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Eliya adasendera pafupi ndi anthu onsewo, naŵafunsa kuti, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iŵiri mpaka liti? Ngati Chauta ndiye Mulungu, mtsateni. Koma ngati Baala ndiye Mulungu, tsatani iyeyo.” Anthuwo sadamuyankhe ndi liwu limodzi lomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliya anapita patsogolo pa anthuwo ndipo anati, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iwiri mpaka liti? Ngati Yehova ndi Mulungu, mutsateni; koma ngati Baala ndi Mulungu, mutsateni.” Koma anthu aja sanayankhe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayika-kayika kufikira liti? ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo anthu nnena kumyankha mau amodzi.