1 Kings 18:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Eliya adauza aneneri a Baala aja kuti, “Yambani ndinu. Sankhulani ng'ombe yamphongo imodzi, muikonze, poti mwachuluka. Tsono mutame dzina la mulungu wanu mopemba, koma musasonkhe moto ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Eliya ananena ndi aneneri a Baala, Dzisankhireni ng'ombe imodzi yanu, muyambe kuikonza, popeza muchuluka; nimuitane dzina la mulungu wanu, koma musasonkhepo moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliya anawuza aneneri a Baala kuti, “Yambani ndinu. Sankhani ngʼombe yayimuna imodzi, muyikonze, popeza mulipo ambiri. Muyitane dzina la mulungu wanu, koma musakoleze moto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Eliya ananena ndi aneneri a Paala, Dzisankhireni ng'ombe imodzi yanu, muyambe kuikonza, popeza mucuruka; nimuitane dzina la mulungu wanu, koma musasonkhepo moto.