1 Kings 18:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzuŵa litapendeka, adakhala akufuulabe mopenga kufikira nthaŵi yoperekera nsembe idakwana. Komabe kunali zii! Osamveka ndi liwu lomwe. Panalibe woyankha, panalibe ndi mmodzi yemwe wosamalako zimenezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wovomereza, kapena wakuwamvera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yamasana inadutsa, ndipo anapitiriza kunenera mwakhama mpaka nthawi yopereka nsembe ya madzulo. Koma panalibe yankho. Palibe amene anayankha, kapena kulabadira zimenezo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wobvomereza, kapena wakuwamvera.