1 Kings 18:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Eliya adauza anthu onse aja kuti, “Senderani pafupi ndi ine.” Anthu onsewo adasenderadi kwa iyeyo. Tsono Eliya adakonza guwa la Chauta limene linali litagwetsedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Eliya ananena ndi anthu onse, Senderani kwa ine; ndipo onse anasendera kwa iye. Iye nakonza guwa la nsembe la Yehova lidagumukalo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Eliya anati kwa anthu onse, “Senderani pafupi ndi ine.” Ndipo anthu onsewo anasendera pafupi ndi iye, ndipo iye anakonza guwa lansembe la Yehova limene linali litawonongeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Eliya ananena ndi anthu onse, Senderani kwa ine; ndipo onse anasendera kwa iye. Iye nakonza guwa la nsembe la Yehova lidagumukalo.