1 Kings 18:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Itakwana nthaŵi yake yopereka nsembe, mneneri Eliya adasendera pafupi ndi guwa nati, “Inu Chauta, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Israele, lero zidziŵike kuti Inuyo ndiye Mulungu m'dziko la Israele, ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, ndiponso kuti ndachita zonsezi chifukwa mwanena ndinu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isaki ndi Israele, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israele, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndachita zonsezi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi yopereka nsembe, mneneri Eliya anasendera pafupi ndi guwa lansembe, napemphera kuti, “Inu Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, lero zidziwike kuti ndinu Mulungu mu Israeli ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, kuti ine ndachita zonsezi chifukwa mwalamula ndinu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isake ndi Israyeli, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israyeli, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndacita zonsezi.