1 Kings 18:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Eliya adaŵauza kuti, “Gwirani aneneri onse a Baala. Asapulumukepo ndi mmodzi yemwe.” Motero adaŵagwira onsewo. Ndipo Eliya adatsikira nawo ku mtsinje wa Kisoni, nakaŵaphera kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Eliya anati kwa iwo, Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense. Nawagwira, ndipo Eliya anapita nao ku mtsinje wa Kisoni, nawapha pamenepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Eliya analamula anthuwo kuti, “Gwirani aneneri a Baala. Musalole kuti wina aliyense athawe!” Anagwira onsewo ndipo Eliya anabwera nawo ku Chigwa cha Kisoni, nawapha kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Eliya anati kwa iwo, Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense. Nawagwira, ndipo Eliya ana pita nao ku mtsinje wa Kisoni, nawapha pamenepo.