1 Kings 18:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adauza mtumiki wake kuti, “Pita ukayang'ane ku nyanja.” Mtumikiyo adapita kukayang'ana, nati, “Kulibe kanthu.” Eliya adamuuza kuti, “Pitanso kasanunkaŵiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa mnyamata wake, Kwera kapenyerere kunyanja. Iye nakwera, napenyetsetsa, nati, Kulibe kanthu. Nati, Bwerezanso kasanu ndi kawiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliya anawuza mtumiki wake kuti, “Pita kayangʼane ku nyanja.” Ndipo iye anapita nakayangʼana. Mtumikiyo anati, “Kulibe kanthu.” Kasanu nʼkawiri Eliya anati, “Pitanso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa mnyamata wace, Kwera kapenyerere kunyanja. Iye nakwera, napenyetsetsa, nati, Kulibe kanthu. Nati, Bwerezanso kasanu ndi kawiri.