1 Kings 18:44 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtumikiyo atapita kachisanu ndi chiŵiri adati, “Pali kamtambo kakang'ono konga dzanja la munthu, kakutuluka kunyanjako.” Pompo Eliya adati, “Pita kamuuze Ahabu kuti akonze galeta lake, ndipo azipita, kuti mvula ingamtsekereze.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali kachisanu ndi chiwiri anati, Taonani, kwatuluka kunyanja kamtambo konga dzanja la munthu. Nati iye, Kauze Ahabu, kuti, Mangani galeta, tsikani, mvula ingakutsekerezeni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ulendo wachisanu ndi chiwiri mtumikiyo anafotokoza kuti, “Taonani, kamtambo kakangʼono kokhala ngati dzanja la munthu kakutuluka ku nyanja.” Pamenepo Eliya anati, “Pita, kamuwuze Ahabu kuti, ‘Konzani galeta lanu ndipo mutsike mvula isanakutsekerezeni.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali kacisanu ndi ciwiri anati, Taonani, kwaturuka kunyanja kamtambo konga dzanja la munthu. Nati iye, Kauze Ahabu, kuti, Mangani gareta, tsikani, mvula Ingakutsekerezeni.