1 Kings 18:45 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Posachedwa kuthambo kudangoti bii ndi mitambo, mphepo idaomba ndipo padagwa mvula yaikulu. Ahabu adakwera galeta napita ku Yezireele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, polinda kanthawi, thambo linada ndi mitambo ndi mphepo, nigwa mvula yaikulu. Ndipo Ahabu anayenda m'galeta, namuka ku Yezireele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyi nʼkuti kuthambo kutayamba kusonkhana mitambo yakuda, mphepo inawomba, mvula yamphamvu inagwa ndipo Ahabu anakwera galeta napita ku Yezireeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, polinda kanthawi, thambo linada ndi mitambo ndi mphepo, nigwa mvula yaikuru. Ndipo Ahabu anayenda m'gareta, namuka ku Yezreeli.