1 Kings 18:46 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mphamvu za Chauta zinali naye Eliya. Iyeyo adakwinda chovala chake, nathamanga mwaliŵiro, nkupitirira Ahabu mpaka adayambira ndiye kukafika ku chipata cha ku Yezireele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dzanja la Yehova linakhala pa Eliya; namanga iye za m'chuuno mwake, nathamanga m'tsogolo mwa Ahabu ku chipata cha Yezireele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzanja la Yehova linali pa Eliya ndipo atamangira lamba chovala chake, anathamanga ndi kumupitirira Ahabu mpaka kukhala woyamba kukafika ku Yezireeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dzanja la Yehova tinakhala pa Eliya; namanga iye za m'cuuno mwace, nathamanga m'tsogolo mwa Ahabu ku cipata ca Yezreeli.