1 Kings 19:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Eliya adayankha kuti, “Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, ineyo ndakhala ndikutumikira Inu nokha nthaŵi zonse. Koma anthu a ku Israele aphwanya chipangano chimene adachita ndi Inu, ndipo agwetsa maguwa anu ndi kupha aneneri anu ndi lupanga. Ineyo ndangotsala ndekha. Tsono akufunafunanso moyo wanga, kuti andiphe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Ine ndinachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele anasiya chipangano chanu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Ndakhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Aisraeli asiya pangano lanu, agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga. Ndatsala ine ndekha ndipo tsopano akufuna kundipha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Ine ndinacitira cangu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israyeli anasiya cipangano canu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuucotsa.