1 Kings 19:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Chauta adati, “Tuluka, ukaime pa phiri, pamaso panga.” Tsono Chauta adadutsa pamenepo, ndipo mphepo yamphamvu idaomba ning'amba mapiri ndi kuswa matanthwe, koma Chauta sanali m'mphepomo. Itapita mphepoyo, padachita chivomezi, koma Chauta sanali m'chivomezimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime pa phiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m'chivomezicho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati, “Tuluka ndipo ukayime pa phiri pamaso pa Yehova, pakuti Yehova ali pafupi kudutsa pamenepo.” Tsono mphepo yayikulu ndi yamphamvu inawomba ningʼamba mapiri ndi kuswa matanthwe pamaso pa Yehova, koma Yehova sanali mʼmphepomo. Itapita mphepoyo panachita chivomerezi, koma Yehova sanali mʼchivomerezicho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anati, Turuka, nuime pa phiri tino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikuru ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhala m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali cibvomezi; komanso Yehova sanali m'cibvomezico.