1 Kings 19:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Eliya atakamva, adafunda kumutu, ndipo adatuluka, nakaima pa khomo la phanga. Pomwepo padamveka mau omuuza kuti, “Ukuchita chiyani kuno, iwe Eliya?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atamva Eliya, anafunda nkhope yake ndi chofunda chake, natuluka, naima pa khomo la phangalo. Ndipo taonani, anamdzera mau akunena naye, Uchitanji kuno, Eliya?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliya atamva kamphepoko, anakokera chovala chake naphimba kumutu. Anatuluka ndipo anayima pa khomo la phanga. Ndipo panamveka mawu akuti, “Eliya, ukuchita chiyani kuno?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atamva Eliya, anapfunda nkhope yace ndi copfunda cace, naturuka, naima pa khomo la phangalo. Ndipo taonani, anamdzera mau akunena naye, Ucitanji kuno, Eliya?