1 Kings 19:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Eliya adamuyankha kuti, “Chabwino, pita. Ndakuletsa ngati?” Apo Elisa adabwerera, ndipo adatenga ng'ombe zake ziŵiri nazipha. Kenaka adatenga magoli a ng'ombezo nasonkhera moto nkuphikira nyamayo, ndipo adaipereka kwa anthu kuti adye. Pambuyo pake adanyamuka namayenda ndi Eliya ndi kumamtumikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yake ndi zipangizo za zochitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Elisa anamusiya Eliyayo nabwerera kwawo. Anatenga ngʼombe zake ziwiri zapagoli nazipha. Anatenga magoli a mapulawo ake nasonkhera moto kuphikira nyamayo ndipo anayipereka kwa anthu kuti adye. Ndipo ananyamuka natsatira Eliya ndi kukhala mtumiki wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yace ndi zipangizo za zocitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.