1 Kings 19:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Eliya mwini wake adayenda ulendo wa tsiku limodzi m'chipululu, nakakhala pansi patsinde pa kamtengo ka tsache. Tsono adapempha kuti afe, adati, “Zandikola! Inu Chauta, bwanji ndingofa basi! Ine sindingapambane makolo anga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iye mwini analowa m'chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo Eliyayo anayenda ulendo wa tsiku limodzi mʼchipululu. Anafika pa kamtengo ka tsache, nakhala pansi pa tsinde lake napemphera kuti afe. Iye anati, “Yehova, ine ndatopa nazo. Chotsani moyo wanga. Ineyo sindine wopambana makolo anga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye mwini analowa m'cipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, cotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindiri wokoma woposa makolo anga.