1 Kings 19:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Eliya uja adadzuka, nadya nkumwera. Motero adapeza mphamvu zoyendera. Adayenda masiku makumi anai usana ndi usiku mpaka adakafika ku Sinai, phiri la Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvu ya chakudya chimenecho masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika kuphiri la Mulungu ku Horebu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Eliya anadzuka nadya ndi kumwa. Atapeza mphamvu chifukwa cha chakudyacho, anayenda masiku 40, usana ndi usiku mpaka anafika ku Horebu, phiri la Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvuya cakudya cimeneco masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika ku phiri la Mulungu ku Horebu.