1 Kings 19:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumeneko adafikira m'phanga, nagona momwemo. Tsono Chauta adadzamuuza kuti, “Ukuchitako chiyani kuno, iwe Eliya?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nafika kuphanga, nagona kumeneko, ndipo taonani, mau a Yehova anamfikira, nati kwa iye, Uchitanji pano, Eliya?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumeneko analowa mʼphanga, nakhala komweko. Ndipo taonani, Yehova anayankhula naye kuti, “Eliya, ukuchita chiyani kuno?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nafika kuphanga, nagona kumeneko, ndipo taonani, mau a Yehova anamfikira, nati kwa iye, Ucitanji pano, Eliya?