1 Kings 2:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo nkuti atalamulira Israele zaka makumi anai. Ku Hebroni adalamulira zaka zisanu ndi ziŵiri, ndipo ku Yerusalemu zaka 33.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo masiku ake akukhala Davide mfumu ya Israele anali zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu ku Hebroni, ndi zaka makumi atatu mphambu chitatu anakhala mfumu ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyeyo nʼkuti atalamulira Israeli kwa zaka makumi anayi. Ku Hebroni analamulira zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo masiku ace akukhala Davide mfumu ya Israyeli anali zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu ku Hebroni, ndi zaka makumi atatu mphambu citatu anakhala mfumu ku Yerusalemu.