1 Kings 2:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Adoniya, mwana wa Hagiti, adafika kwa Bateseba, mai wake wa Solomoni. Bateseba adamufunsa kuti, “Kodi wadzera mtendere?” Iye adati, “Ai, ndi zamtendere ndithu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Adoniya mwana wa Hagiti anadza kwa Bateseba amai wake wa Solomoni, ndipo mkaziyo anati, Kodi wadza ndi mtendere? Nati, Ndi mtendere umene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Adoniya, mwana wa Hagiti, anapita kwa Batiseba, amayi ake a Solomoni. Batiseba anamufunsa kuti, “Kodi wabwera mwamtendere?” Iye anayakha kuti, “Eya, ndi zamtendere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Adoniya mwana wa Hagati anadza kwa Batiseba amai wace wa Solomo, ndipo mkaziyo anati, Kodi wadza ndi mtendere? Nati, Ndi mtendere umene.