1 Kings 2:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adoniya adati, “Mukudziŵa kuti ufumuwu udaali wanga, ndipo Aisraele onse ankayembekeza kuti ndidzalamulira ndine. Koma zinthu zatembenuka, ufumuwo wapita kwa mbale wanga, popeza kuti adampatsa ndi Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Mudziwa kuti ufumu unali wanga, ndi kuti Aisraele onse anaika maso ao pa ine, kuti ndikhale mfumu ndine; koma ufumu watembenuka nukhala wa mbale wanga, popeza iye anaulandira kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Adoniya anati, “Monga inu mukudziwa, ufumu unali wanga. Aisraeli onse ankayembekezera kuti ine ndidzakhala mfumu yawo. Koma zinthu zinasintha ndipo ufumu wapita kwa mʼbale wanga; pakuti wapatsa iye ufumuwu ndi Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Mudziwa kuti ufumu unali wanga, ndi kuti Aisrayeli onse anaika maso ao pa ine, kuti ndikhale mfumu ndine; koma ufumu watembenuka nukhala wa mbale wanga, popeza iye anaulandira kwa Mulungu.