1 Kings 2:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Bateseba adapita kwa mfumu Solomoni kukalankhula naye m'malo mwa Adoniya. Solomoni adanyamuka kuti akumane naye, ndipo adaŵeramira mai wakeyo. Adakhala pa mpando wake waufumu, ndipo adaitanitsa mpando wina kuti mai wake akhalepo. Tsono mai uja adakhala ku dzanja lamanja la mfumuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono Bateseba ananka kwa mfumu Solomoni kukanenera Adoniya kwa iye. Ndipo mfumu inanyamuka kukomana naye, namuweramira nakhalanso pa mpando wake wachifumu, naikitsa mpando wina wa amake wa mfumu, nakhala iye ku dzanja lake lamanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Batiseba atapita kwa Mfumu Solomoni kukayankhula naye mʼmalo mwa Adoniya, mfumu inanyamuka kukumana naye, ndipo inaweramira amayi akewo, kenaka inakhala pa mpando wake waufumu. Iye anayitanitsa mpando wina kuti amayi ake akhalepo ndipo anakhala pansi ku dzanja lake lamanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono Batiseba ananka kwa mfumu Solomo kukanenera Adoniya kwa iye. Ndipo mfumu inanyamuka kukomana naye, namuweramira nakhalanso pa mpando wace wacifumu, naikitsa mpando wina wa amace wa mfumu, nakhala iye ku dzanja lace lamanja.