1 Kings 2:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Solomoni adafunsa mai wakeyo kuti, “Chifukwa chiyani mukumpemphera Abisagi Msunamu Adoniyayu? Mpemphereninso ndi ufumu womwe, poti iyeyu ndi mkulu wanga, ndipo akugwirizana ndi wansembe Abiyatara ndiponso Yowabu mwana wa Zeruya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Solomoni anayankha, nati kwa amai wake, Mupempheranji Abisagi wa ku Sunamu akhale wake wa Adoniya? Mumpempherenso ufumu, popeza ndiye mkulu wanga; inde ukhale wake, ndi wa Abiyatara wansembeyo, ndi wa Yowabu mwana wa Zeruya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mfumu Solomoni inayankha amayi ake aja kuti, “Chifukwa chiyani mukupemphera Adoniya Abisagi wa ku Sunemu? Mungathenso kumupemphera ufumu pakuti iyeyu ndi mkulu wanga ndipo mupemphereninso wansembe Abiatara ndi Yowabu mwana wa Zeruya!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Solomo anayankha, nati kwa amai wace, Mupempheranji Abisagi wa ku Sunamu akhale wace wa Adoniya? Mumpempherenso ufumu, popeza ndiye mkuru wanga; inde ukhale wace, ndi wa Abyatara wansembeyo, ndi wa Yoabu mwana wa Zeruya.