1 Kings 2:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake, pali Chauta wamoyo, amene adandisankhula ndi kundikhazika pa mpando waufumu wa Davide bambo wanga, nandipatsa ufumuwu monga momwe adalonjezera, Adoniya aphedwa ndithu lero lomwe lino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsono, pali Yehova amene wandikhazikitsa ine, nandikhalitsa pampando wachifumu wa Davide atate wanga, nandimangira nyumba monga analonjeza, zedi Adoniya aphedwa lero lomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono pali Yehova wamoyo, amene anandikhazikitsa ine pa mpando waufumu wa abambo anga Davide ndi kundipatsa ufumu monga analonjezera, Adoniya aphedwa lero lomwe lino!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsono, pali Yehova amene wandikhazikitsa ine, nandikhalitsa pampando wacifumu wa Davide atate wanga, nandimangira nyumba monga analonjeza, zedi Adoniya aphedwa lero lomwe.