1 Kings 2:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yowabu adamva zimenezi, adathaŵira ku hema lopatulika la Chauta nakagwira nsonga za guwa lansembe. Yowabu ndiye uja ankathandiza Adoniya koma osati Abisalomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mbiriyi inamfika Yowabu, pakuti Yowabu anapatukira kwa Adoniya, angakhale sanapatukire kwa Abisalomu. Ndipo Yowabu anathawira ku chihema cha Yehova, nagwira nyanga za guwa la nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yowabu atamva zimenezi anathawira ku tenti ya Yehova ndipo anakagwira msonga za guwa lansembe, popeza Yowabu ndiye anathandiza Adoniya kuwukira koma sanathandize Abisalomu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mbiriyi inamfika Yoabu, pakuti Yoabu anapambukira kwa Adoniya, angakhale sanapambukira kwa Abisalomu. Ndipo Yoabu anathawira ku cihema ca Yehova, nagwira nyanga za guwa la nsembe.