1 Kings 2:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mfumu Solomoni atamva kuti Yowabu wathaŵira ku hema la Chauta, ndipo kuti wakhala pambali pa guwa lansembe, adatuma Benaya mwana wa Yehoyada namuuza kuti, “Pita, ukamuphe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuuza mfumu Solomoni, kuti, Yowabu wathawira ku chihema cha Yehova; ndipo taonani, wakhala ku guwa la nsembe. Pomwepo Solomoni anatuma Benaya mwana wa Yehoyada, nati, Kamkwere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Solomoni inawuzidwa kuti Yowabu wathawira ku tenti ya Yehova ndipo ali pambali pa guwa lansembe. Tsono Solomoni analamula Benaya mwana wa Yehoyada kuti, “Pita, kamukanthe!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuuza mfumu Solomo, kuti, Yoabu wathawira ku cihema ca Yehova; ndipo taonani, wakhala ku guwa la nsembe. Pomwepo Solomo anatuma Benaya mwana wa Yehoyada, nati, Kamkwereo