1 Kings 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uzichita zimene Chauta Mulungu wako akulamula. Uziyenda m'njira za Chauta, uzimvera mau, malangizo ndi malamulo a Mulungu, monga momwe adalembedwera m'malamulo a Mose, kuti zonse zizikuyendera bwino kulikonse kumene ungapite.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nusunge chilangizo cha Yehova Mulungu wako, kuyenda m'njira zake, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wake, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose, kuti ukachite mwa nzeru m'zonse ukachitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo uzichita zimene Yehova Mulungu wako amafuna, uziyenda mʼnjira zake, uzisunga malangizo ndi malamulo ake monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo a Mose, kuti zonse zimene udzachite zidzakuyendere bwino kulikonse kumene udzapite.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nusunge cilangizo ca Yehova Mulungu wako, kuyenda m'njira zace, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wace, monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose, kuti ukacite mwa nzeru m'zonse ukacitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako;