1 Kings 2:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Benaya adapita ku hema la Chauta lija, ndipo adauza Yowabuyo kuti, “Mfumu ikukulamula kuti utuluke.” Koma Yowabuyo adati, “Iyai, ine ndifera pompano.” Apo Benaya adakauzanso mfumu zimene Yowabu adaanena.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nafika Benaya ku chihema cha Yehova, nati kwa iye, Mfumu itero, Tatuluka. Nati, Iai, koma ndifere pompano. Ndipo Benaya anabweza mau kwa mfumu, nati, Yowabu wanena chakuti, nandiyankha mwakutimwakuti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Benaya analowa mʼtenti ya Yehova ndipo anati kwa Yowabu, “Mfumu ikuti ‘Tuluka!’ ” Koma iye anayankha kuti, “Ayi, ine ndifera muno.” Benaya anakafotokozera mfumu kuti, “Umu ndi mmene Yowabu wandiyankhira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nafika Benaya ku cihema ca Yehova, nati kwa iye, Mfumu itero, Taturuka. Nati, Iai, koma ndifere pompano. Ndipo Benaya anabweza mau kwa mfumu, nati, Yoabu wanena cakuti, nandiyankha mwakuti mwakuti.