1 Kings 2:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu idamuyankha kuti, “Kachite monga momwe iye waneneramo. Ukamuphe, ndipo ukamuike m'manda. Motero udzandichotsera ine pamodzi ndi banja la bambo wanga mlandu wa imfa ya anthu amene Yowabu adaŵapha popanda chifukwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inati kwa iye, Chita monga umo wanena iye, numkwere, numuike; kuti undichotsere ine ndi nyumba ya atate wanga mwazi uja Yowabu anaukhetsa wopanda chifukwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mfumu inalamula Benaya kuti, “Kachite monga iye wanenera. Ukamukanthe ndi kumuyika mʼmanda. Ukatero udzandichotsera ine pamodzi ndi nyumba ya abambo anga mlandu wa anthu osalakwa amene Yowabu anawapha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inati kwa iye, Cita monga umo wanena iye, numkwere, numuike; kuti undicotsere ine ndi nyumba ya atate wanga mwazi uja Yoabu anaukhetsa wopanda cifukwa.