1 Kings 2:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzambwezera ntchito zake zokhetsa magazi chifukwa choti iye adapha ndi lupanga anthu abwino aŵiri aja amene anali osalakwa kupambana iyeyo, bambo wanga Davide osadziŵa. Anthu aŵiriwo ndiwo Abinere mwana wa Nere ndi mtsogoleri wa ankhondo a ku Israele, ndiponso Amasa mwana wa Yetere mtsogoleri wa ankhondo a ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pa mutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzamubwezera zomwe anachita pokhetsa magazi, chifukwa iye anakantha ndi lupanga anthu awiri abwino ndi olungama kuposa iye, nawapha, abambo anga Davide osadziwa. Anthu awiriwo ndi Abineri mwana wa Neri, wolamulira gulu lankhondo la Israeli ndi Amasa mwana wa Yeteri, wolamulira gulu lankhondo la Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wace pa mutu wace wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abineri mwana wa Neri kazembe wa khamu la nkhondo la Israyeli, ndi Amasa mwana wa Yeteri kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.