1 Kings 2:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho chilango cha magazi omwe adakhetsa aja chibwerere pa Yowabu ndiponso pa zidzukulu zake mpaka muyaya. Koma mtendere wochokera kwa Chauta ukhale pa Davide ndi zidzukulu zake, pa banja lake ndi pa mpando wake waufumu, mpaka muyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero mwazi wao udzabweranso pa mutu wake wa Yowabu, ndi pa mutu wa mbumba yake, ku nthawi yamuyaya; koma Davide, ndi mbumba yake, ndi banja lake, ndi mpando wake wachifumu adzakhala ndi mtendere wa Yehova ku nthawi yamuyaya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Magazi amene Yowabu anakhetsa akhale pamutu pake ndi pa zidzukulu zake kwamuyaya. Koma pa Davide ndi zidzukulu zake, nyumba yake ndi mpando wake waufumu pakhale mtendere wochokera kwa Yehova kwamuyaya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero mwazi wao udzabweranso pa mutu wace wa Yoabu, ndi pa mutu wa mbumba yace, ku nthawi yamuyaya; koma Davide, ndi mbumba yace, ndi banja lace, ndi mpando wace wacifumu adzakhala ndi mtendere wa Yehova ku nthawi yamuyaya.