1 Kings 2:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu idaika Benaya mwana wa Yehoyada kuti aziyang'anira gulu lankhondo m'malo mwa Yowabu, ndipo idaika wansembe Zadoki m'malo mwa Abiyatara.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inaika Benaya mwana wa Yehoyada m'malo mwake kutsogolera khamu la nkhondo, ndi mfumu inaika Zadoki wansembe m'malo mwa Abiyatara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inayika Benaya mwana wa Yehoyada kuti akhale woyangʼanira gulu lankhondo mʼmalo mwa Yowabu ndipo inayika Zadoki kuti akhale wansembe mʼmalo mwa Abiatara.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inaika Benaya mwana wa Yehoyada m'malo mwace kutsogolera khamu la nkhondo, ndi mfumu inaika Zadoki wansembe m'malo mwa Abyatara.