1 Kings 2:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mfumu idatuma anthu kukaitana Simei, ndipo atabwera, idamuuza kuti, “Umange nyumba yako muno mu Yerusalemu, ndipo uzikhala mommuno, osamatuluka kukayenda kwina kulikonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simei, nati kwa iye, Udzimangire nyumba m'Yerusalemu, nukhale komweko osatulukako kunka kwina konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mfumu inatuma anthu kukayitana Simei ndipo inamuwuza kuti, “Udzimangire nyumba mu Yerusalemu ndipo uzikhala kumeneko, koma usatuluke mu mzinda kupita kwina kulikonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simeyi, nati kwa iye, Udzimangire nyumba m'Yerusalemu, nukhale komweko osaturukako kumka kwina konse.