1 Kings 2:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simei adauza mfumu kuti, “Zimene mukunenazi nzabwino. Ine kapolo wanu ndidzachita monga momwe mwaneneramu, mbuyanga mfumu.” Choncho Simei adakhala mu Yerusalemu masiku ambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Simei anena ndi mfumu, Mau awa ndi abwino; monga momwe mwanena mbuye wanga mfumu momwemo ndidzachita kapolo wanu. Ndipo Simei anakhala m'Yerusalemu masiku ambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Simei anayankha mfumu kuti, “Zimene mwanenazi nʼzabwino. Kapolo wanu adzachita monga mbuye wanga mfumu mwanenera.” Choncho Simei anakhala mu Yerusalemu nthawi yayitali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Simeyi ananena ndi mfumu, Mau awa ndi abwino; monga momwe mwanena mbuye wanga mfumu momwemo ndidzacita kapolo wanu. Ndipo Simeyi anakhala m'Yerusalemu masiku ambiri.