1 Kings 2:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma zidangotere kuti patapita zaka zitatu, akapolo aŵiri a Simei adaathaŵira kwa Akisi, mwana wa Maaka, mfumu ya ku Gati. Simei atamva kuti akapolo ake ali ku Gati,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika, zitapita zaka zitatu, kuti akapolo awiri a Simei anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka mfumu ya Gati. Ndipo anamuuza Simei, nati, Taonani, akapolo anu akhala ku Gati.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma patatha zaka zitatu, akapolo awiri a Simei anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka, mfumu ya ku Gati, ndipo Simei anawuzidwa kuti, “Akapolo anu ali ku Gati.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika, zitapita zaka zitatu, kuti akapolo awiri a Simeyi anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka mfumu ya Gati. Ndipo anamuuza Simeyi, nati, Taonani, akapolo anu akhala ku Gati.