1 Kings 2:42 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
adamuitanitsa Simeiyo namufunsa kuti, “Kodi sindidakulumbiritse iwe m'dzina la Chauta ndi kukuchenjeza kwathunthu kuti tsiku limene udzatuluke ndi kupita kwina kulikonse, udzaphedwa? Ndipo iwe udaandiwuza kuti, ‘Zimene mwanenazi nzabwino, ndimvera.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simei, niti kwa iye, Kodi sindinakulumbiritsa pa Yehova ndi kukuchenjeza, kuti, Tadziwa ndithu, kuti tsiku lakutuluka iwe ndi kukayenda kwina konse udzafa ndithu? Ndipo iwe unati kwa ine, Mau amene ndawamva ndi abwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mfumu inamuyitanitsa Simei ndipo inamufunsa kuti, “Kodi sindinakulumbiritse mʼdzina la Yehova ndi kukuchenjeza kuti, ‘Tsiku limene udzatuluka kupita kwina kulikonse, udziwe kuti udzafa’? Nthawi imeneyo iwe unandiwuza kuti, ‘Zimene mwanena nʼzabwino. Ine ndidzamvera.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simeyi, niti kwa iye, Kodi sindinakulumbiritsa pa Yehova ndi kukucenjeza, kuti, Tadziwa ndithu, kuti tsiku lakuturuka iwe ndi kukayenda kwina konse udzafa ndithu? Ndipo iwe unati kwa ine, Mau amene ndawamva ndi abwino.