1 Kings 2:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu idauzanso Simei kuti, “Ukudziŵa mumtima mwakomo zoipa zonse zimene udamchita Davide, bambo wanga. Tsopano Chauta akubwezera zoipa zako pa iwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono mfumu inanenanso ndi Simei Udziwa iwe choipa chonse mtima wako umadziwacho, chimene udachitira Davide atate wanga; chifukwa chake Yehova adzakubwezera choipa chako pamutu pako mwini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumuyo inawuzanso Simei kuti, “Ukudziwa mu mtima mwakomo zoyipa zonse zimene unachitira abambo anga Davide. Tsopano Yehova akubwezera zoyipa zakozo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono mfumu inanenanso ndi Simeyi, Udziwa iwe coipa conse mtima wako umadziwaco, cimene udacitira Davide atate wanga; cifukwa cace Yehova adzakubwezera coipa cako pamutu pako mwini.