1 Kings 2:46 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo mfumuyo idalamula Benaya mwana wa Yehoyada. Ndipo iye adatuluka nakamupha Simeiyo. Motero ufumu wa Solomoni udakhazikikadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu inalamulira Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye anatuluka namkwera, namwalira iye. Ndipo ufumu unakhazikika m'dzanja la Solomoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mfumu inalamula Benaya mwana wa Yehoyada ndipo iye anapita kukakantha Simei ndi kumupha. Tsono ufumu unakhazikika mʼdzanja la Solomoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu inalamulira Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye anaturuka namkwera, namwalira iye. Ndipo ufumu unakhazikika m'dzanja la Solomo.