1 Kings 2:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kuwonjezera pamenepo, ukudziŵanso zoipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya adandichita, pakupha atsogoleri aŵiri a ankhondo a Aisraele aja, Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere. Kuteroko kunali kulipsira pa nthaŵi yamtendere magazi amene anthuwo adaakhetsa pa nthaŵi yankhondo. Koma tsopano ine pokhala mfumu, ndikusenza kuchimwa kwake ndi kuvala mlandu chifukwa cha magazi osachimwawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso udziwa chimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, inde chimene anawachitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israele, ndiwo Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lake la m'chuuno mwake, ndi pa nsapato za pa mapazi ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono iwe ukudziwanso zoyipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira pakupha atsogoleri awiri a ankhondo a Israeli, Abineri mwana wa Neri ndi Amasa mwana wa Yeteri. Iye anawapha ndi kukhetsa magazi nthawi ya mtendere ngati nthawi ya nkhondo, ndipo anapaka magazi amenewo pa lamba wa mʼchiwuno mwake ndi pa nsapato za ku mapazi ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso udziwa cimene Yoabu mwana wa Zeruya anandicitira, inde cimene anawacitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israyeli, ndiwo Abineri mwana wa Neri, ndi Amasa mwana wa Yeteri, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lace la m'cuuno mwace, ndi pa nsapato za pa mapazi ace.