1 Kings 2:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi, uŵachitire zabwino ndi kuŵalola kuti azidya pamodzi nawe, poti adandichitira chifundo pamene adakumana nane nthaŵi imene ndinkathaŵa Abisalomu mbale wako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma uchitire zokoma ana amuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi uwakomere mtima ndipo uwalole kuti akhale mʼgulu la anthu amene azidya pamodzi nawe. Pakuti anandisamalira pamene ndinkathawa mʼbale wako Abisalomu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ucitire zokoma ana amuna aja a Barizilai wa ku Gileadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.