1 Kings 20:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, adasonkhanitsa magulu ake onse ankhondo, ndipo adagwirizana ndi mafumu ena 32 okhala ndi akavalo ndi magaleta. Iyeyo ndi mafumu anzakewo adapita ndipo adakazinga mzinda wa Samariya nauthira nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magaleta; nakamangira Samariya misasa, naponyana nao nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu inasonkhanitsa magulu ake onse a ankhondo. Iye pamodzi ndi mafumu 32, akavalo awo ndi magaleta awo, anapita kukawuzungulira mzinda wa Samariya ndi kuwuthira nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lace lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magareta; nakamangira Samaria misasa, naponyana nao nkhondo.