1 Kings 20:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Benihadadi adatumizanso mau kwa Ahabu kuti, “Ndibwera ndi anthu anga ambiri kudzaononga mzinda wakowo, ndipo adzausandutsa fumbi lokhalokha. Milungu indilange ngati ndilephera kuchita zimenezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati fumbi la Samariya lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Beni-Hadadi anatumizanso uthenga wina kwa Ahabu kuti, “Milungu indilange koopsa, ngati mu Samariya mudzakhale fumbi loti nʼkudzaza dzanja la aliyense wa anthu anga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati pfumbi la Samaria lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.