1 Kings 20:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Benihadadi adamva mau ameneŵa, pamene ankamwa pamodzi ndi mafumu anzake aja m'mahema, tsono adauza anthu ake aja kuti, “Konzekerani nkhondo.” Ndipo anthuwo adakonzekera kuuthira nkhondo mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika, atamva Benihadadi mau awa, analikumwa nao mafumu m'misasa, ananena ndi anyamata ake, Nikani. Nandandalika pamudzipo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Beni-Hadadi anamva uthenga umenewu pamene iye ankamwa ndi mafumu anzake mʼmatenti awo, ndipo analamula anthu ake kuti, “Konzekerani kukathira nkhondo.” Choncho anakonzekera kukathira nkhondo mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika, atamva Benihadadi mau awa, analikumwa nao mafumu m'misasa, ananena ndi anyamata ace, Nikani. Nandandalika pamudzipo.