1 Kings 20:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo mneneri wina adadza kwa Ahabu, mfumu ya ku Israele, namuuza mau a Chauta akuti, “Kodi ukuchiwona chigulu cha ankhondochi? Ndithudi ndikuchipereka chigulu chimenechi m'manja mwako lero lino. Motero udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taonani, mneneri anadza kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukulu wonse? Taonani, ndidzaupereka m'dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo taonani, mneneri wina anabwera kwa Ahabu mfumu ya Israeli nadzalengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi ukuchiona chigulu chachikulu cha ankhondochi? Taona, ndikuchipereka chimenechi lero mʼdzanja lako, ndipo pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taonani, mneneri anadza kwa Ahabu mfumu ya Israyeli, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukuru wonse? Taonani, ndidzaupereka m'dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova.