1 Kings 20:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ahabu adafunsa kuti, “Kodi zimenezo zidzachitika ndi yani?” Mneneriyo adati, “Chauta akuti zidzachitika ndi ankhondo a nduna zam'maboma.” Ahabu adafunsanso kuti, “Nanga amene adzayambe nkhondoyo ndani?” Mneneriyo adati, “Iweyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Ahabu, Mwa yani? Nati, Atero Yehova, Mwa anyamata a akalonga a madera. Natinso, Adzayamba kuponya nkhondo ndani? Nati, Iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahabu anafunsa kuti, “Koma ndani adzachita zimenezi?” Mneneri anayankha kuti, “Yehova akuti, ‘Adzachita zimenezi ndi asilikali a nduna za mʼzigawo.’ ” Ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndani adzayambe nkhondoyi?” Mneneriyo anayankha kuti, “Ndinu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Ahabu, Mwa yam? Nati, Atero Yehova, Mwa anyamata a akalonga a madera. Natinso, Adzayamba kuponya nkhondo ndani? Nati, Iwe.