1 Kings 20:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatuluka masana nthaŵi imene Benihadadi ndi mafumu 32 othandizana nawo aja ankamwa mpaka kuledzera m'mahema mwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amenewo anatuluka usana. Koma Benihadadi analinkumwa naledzera m'misasamo, iye ndi mafumu aja makumi atatu mphambu awiri aja akumthandiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo ananyamuka nthawi yamasana pamene Beni-Hadadi ndi mafumu 32 othandizana naye ankamwa mpaka kuledzera mʼmatenti awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amenewo anaturuka usana. Koma Benihadadi analinkumwa naledzera m'misasamo, iye ndi mafumu aja makumi atatu mphambu awiri aja akumthandiza.