1 Kings 20:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankhondo a nduna zam'maboma aja, ndiwo amene adayamba kupita ku nkhondo. Nthaŵi yomweyo Benihadadi adatuma anthu oti akazonde. Iwo adadzamuuza kuti, “Kukubwera ankhondo kuchokera ku Samariya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anyamata a akalonga a madera anayamba kutuluka, koma Benihadadi anatuma anthu, iwo nambwezera mau, kuti, M'Samariya mwatuluka anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndiwo amene anayamba kupita ku nkhondo. Nthawi imeneyi Beni-Hadadi nʼkuti atatumiza anthu oti akazonde, amene anadzafotokoza kuti, “Anthu ankhondo akubwera kuchokera ku Samariya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anyamata a akalonga a madera anayamba kuturuka, koma Benihadadi anatuma anthu, iwo nambwezera mau, kuti, M'Samaria mwaturuka anthu.