1 Kings 20:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mneneri uja adadzanso kwa Ahabu, mfumu ya ku Israele, namuuza kuti, “Tiyeni, valani chamuna, ndipo muganize bwino zoti mudzachite. Pakuti chaka chikudzachi, mfumu ya ku Siriya idzabweranso kudzamenyana nanu nkhondo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mneneri uja anayandikira kwa mfumu ya Israele, nati kwa iye, Kadzilimbitseni, mudziwe muchenjere ndi chimene muchichita; popeza chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzabweranso kulimbana nanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitachitika izi, mneneri wina anabwera kwa mfumu ya Israeli ndipo anati, “Mulimbike ndipo muganize bwino zoti mudzachite, chifukwa chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzakuthiraninso nkhondo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mneneri uja anayandikira kwa mfumu ya Israyeli, nati kwa iye, Kadzilimbitseni, mudziwe mucenjere ndi cimene mucicita; popeza caka cikudzaci mfumu ya Aramu idzabweranso kulimbana nanu.