1 Kings 20:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwao kuja akuluakulu a mfumu ya ku Siriya adauza mfumu yao kuti, “Milungu ya anthu a ku Israele ndi milungu yam'mapiri, nchifukwa chake anali ndi mphamvu zotipambanira ife. Koma tiyeni tikamenyane nawo ku chigwa, ndithudi tidzaŵapambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anyamata a mfumu ya Aramu anati kwa iye, Milungu yao nja kumapiri, ndimo m'mene atilakira; koma tikaponyana nao kuchidikha, zedi tidzaposa mphamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyi, akuluakulu a mfumu ya Aramu anamulangiza kuti, “Milungu ya anthu a ku Israeli ndi milungu ya mʼmapiri. Nʼchifukwa chake anali ndi mphamvu zotipambana ife. Koma ngati tidzamenyana nawo ku chigwa, ndithudi ife tidzakhala ndi mphamvu kuposa iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anyamata a mfumu ya Aramu anati kwa iye, Milungu yao nja kumapiri, ndimo m'mene atilakira; koma tikaponyana nao kucidikha, zedi tidzaposa mphamvu.